Mluvčí: Dominic

Jazyk Čičevština, nyanja wiki ethnologue
Nigerokonžská jazyková rodina wiki
latinské písmo scriptsource
Římskokatolická církev wiki

Znamení kříže

Mdzina la Atate, ndi la Mwana ndi la Mzimu Woyera. Amen

Otčenáš

Atate athu muli m'mwamba, dzina lanu liyeretsedwe, ufumu wanu udze, kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba choncho pansi pano.  Mutipatse ife lero chakudya chathu cha lero.  Mutikhululukire ife zochimwa zathu, monga ifenso tiakhululukira adani athu, musatisiye ife m'chinyengo, koma mutipulumutse ife kwa zoyipa. Amen

Zdrávas Maria

Tikuoneni Maria wa chaulele chodzadza, Ambuye ali nanu. Ndinu odala kopambana akazi onse, Ndipo mngodalanso mwana wanu Yesu. Maria oyera amayi a mulungu mutipempherere ife ochimwa, Tsopano ndiponso pa nthawi yakufa kwathu. Amen

Sláva Otci

Ulemu ukhale kwa Atate, ndi kwa Mwana ndi kwa Mzimu Woyera, monga panali poyamba ndi tsopano ndi masiku onse, ndi pa nthawi zosatha. Amen

Apoštolské vyznání víry

Ine ndimvera Mulungu Atate wamphamvu zonse, amene analenga Dziko la kumwamba ndi dziko la pansi pano. Ndipo Yesu Khristu Mwana wake yekha, Ambuye athu, amene anayikidwa m'mimba ndi Mzimu Woyera, nabadwa mwa Maria Virigo, adamsautsa kwa Ponsio Pilato. Adampachika pamtanda, anamwalira, adamuyika m'manda, adalowa m'limbo, ndipo mkuja wake adauka kwa akufa, nakwera kumwamba nakhala padzanja lamanja la Mulungu Atate Amphamvu zonse. Adzafumira komweko kudzaweruza amoyo ndi akufa. Ndipo ndimvera Mzimu Woyera, Eklezia Katolika Woyera, ndimveranso kuti Oyera ayanjana, Mulungu atikhululukira machimo, thupi lidzauka, ulipo moyo osatha. Amen